Bungwe lolimbikitsa nkhani za uchembere wabwino la Mai Khanda Trust lati lili ndi mapulani ofuna kukuza ntchito zake m’dziko muno.
Mkulu woona ntchito za m’bungwe-li a Edward Moses ndi amene wanena izi polankhula ndi mtolankhani wathu amene amafuna kudziwa zambiri zokhudza bungweli.
A Moses ati padakalipano bungweli likugwira ntchito zake m’maboma ena a m’chigawo cha pakati koma liyetsetsa kuti ntchitozi zifalilkire m’dzigawo zonse m’dziko muno.