Zokonzekera mwambo wolonga mfumu ya angoni a kwa njolomole akuti zikuyenda bwino.
Mwambo-wu udzachitika pa 21 September 2017 ku likulu la mfumuyi m’boma la Ntcheu.
Wapampando wa komiti yomwe ikuyendetsa za mwambo-wu Dr keneth wiyo ndi yemwe wanena izi pa 25 August 2017 pa msonkhano wa atolankhani mu m’dzinda wa Blantyre.
Iwo apempha angoni onse m’dziko muno kuti athandize komiti-yi ndi ndalama zoyendetsera mwambowu.
A Wilson Njolomole ndi omwe akukadzodzedwa kukhala inkosi njolomole ndipo izi zichitika kamba koti omwe anali mfumu ya angoni-wa anamwalira chaka chatha