Komiti yomwe ikukonza ulendo wa ku malo oyera a Kibeho m’dziko la Rwanda komwenso kuli mbiri ya bungwe la Divine Mercy Apostolate yati padakalipano zonse zokonzera ulendowu zikuyenda bwino .
Wachiwiri kwa wapampando wa bungweli lomwenso ndi limene lakonza ulendo-wu a Osward Bwemba a ku Chigoneka Catholic Parish mu Arch-Dayosizi ya Lilongwe ati ulendo-wu ulipo pa pa 9 September 2017 ndipo onse amene apite ku malowa adzakabwelelako pa 16 mwezi womwe-wo.
Iwo ati bungwe lawo ndi lokondwa kuti chaka chino, akhristu a mbiri a mpingo wakatolika awonetsa chidwi chopita nawo ku malowa.