Bungwe la Zomba Action Project (Zap) aliyamikira kamba kopeleka thandizo la zipangizo za umoyo ku chipatala chachikulu m’boma la Zomba cha Zomba Central.
Wachiwiri kwa mkulu wa pa chipatala-chi mayi Rose Tchayatchaya ndi omwe anena izi pomwe bungweli limapeleka thandizo la mipando, makina oyezera mano oyenda nawo , ndi zina zambiri pa chipatalachi.
Iwo ati thandizoli labwera mu nthawi yake pomwe chipatalachi chikusowa zambiri pa ntchito zake.
Kotero Iwo apempha kuti mabungwe ndi anthu ena akufuna kwabwino akuyeneranso kufika ndi thandizo lawo ku chipatalachi zomwe zingathandize kupititsa patsogolo ntchito za umoyo pakati pa anthu omwe amafika ndi kudzalandira thandizo lawo pa chipatalachi.
Malingana ndi mkulu wa bungwe la Zomba Action Project (Zap) mayi Nelie Mbano nawo anati bungwe lawo lapeleka thandizo-li mogwilizana ndi bungwe la Colen Action Plan lomwe ndi la m’dziko la Germany.