M’modzi mwa amsembe ampingo wakatolika mu dayosizi ya Chikwawa bambo Mattias George Chiwanda amwalira lachiwiri madzulo atadwala kwa nthawi yochepa.
Malinga ndi akulikulu la mpingo wakatolika kuno ku Malawi mumzinda wa Lilongwe bambo Chiwanda amwalilira pachipatala cha Kalemba mboma la Nsanje.
Malemu Bambo Chiwanda anabadwa pa 12 July mchaka 1969 ndipo amachokera m’mudzi mwa Sorgin mfumu yaikulu Mbenje m’Parishi ya Bangula mboma la Chikwawa.
Malemuwa anazozedwa unsembe pa 16 July mchaka 1995 ku Chikwawa Cathedral ndipo atumikirapo m’ma Parishi a Nsanje, Misomali, Ngabu kuphatikizaponso ndi ku Nsanje Spirituality Centre komanso kusukulu ya asemino ya Mzimu Woyera .
Mwambo woyika m’manda thupi la bambo Chiwanda uchitika pa 20 march ku Chikwawa Cathedral ndipo udzayamba ndi mwambo wa msembe ya misa nthawi ya 9:30 am. Omwe azatsogolere mwambowu ndi episkopi wa dayosiziyi Ambuye Peter Musikuwa.