Anthu awiri amwalira lolemba pa ngozi ziwiri zogundidwa ndi galimoto mboma la Neno.
Malinga ndi mneneri wa apolisi mbomalo a Raphael Kaliati, ngozi yoyamba inachitikira pa msika wa Kanono koma bambo yemwe anamwalira pa ngoziyi pakadali pano sakudziwika dzina lake.
Ngozi ina inachitikira pa msika wa Chifunga pomwe Joseph Wonderson wazaka 22 wa mmudzi mwa Moffat mfumu yayikulu Mlauli mbomalo anawombedwa ndi galimoto. A Kaliati ati anthu onsewa anafera pa malo angozizi ndipo ati mmalo onsewa oyendetsa galimoto anathawa.