Anthu 21 afa nyumba ina yosanjikizana itawagwera mu m’dzinda wa mumbai m’dziko la India.
Malingana ndi malipoti a BBC ambiri mwa anthu omwe afa pa ngozi-yi ndi omwe anali mkati mwa nyumbayi imene inali ndi maofesi a makampani ndi anthu osiyanasiyana m’dzikomo.
Padakalipano nambala ya anthu amene avulala pa ngoziyi siyikudziwika koma kuti ntchito yofufuza ena mwa anthu amene akuwaganizira kuti aphinjidwa ndi zipupa za nyumbayi akuti ili mkati.
Anthu m’dzikomo akuganiza kuti mwina nyumba-yi yagwa kamba ka mvula ya mphamvu yomwe ikupitilira kugwa mmadera osiyanasiyana m’dziko-mo.