Mpingo wakatolika m’dziko la CANADA wati ansembe ampingowu sakuloledwa kutsogolera miyambo ya maliro aanthu amene amwalira mwakufuna kwawo.
Ma-episikopi a mpingo-wu anena izi kudzera mu uthenga wawo. Iwo alankhula izi potsatira kuvomelezedwa kwa lamulo lomwe likupeleka mwayi anthu woti amwalire n gati afuna kutero pa zifukwa zawo.
Pothililapo ndemanga pa nkhaniyi m’modzi mwa ma episcope-wa Arch-Bishop Richard Smith wa arch-dayosizi ya Edmonton wati chiphunzitso cha mpingo sichimavomeleza imfa za mdundu-wu chifukwa ndi imfa zomwe zimadza mosemphana ndi chifuniro cha mulungu.
Iye wati kudzipha ndi m’chitidwe wothandizira imfa ya munthu wina kapena kudzipha kumene ndi zosayenera pamaso pa Mulungu.