Gawo lachiwiri lomanga station ya sitima za pamtunda ya NKAYA m’boma la BALAKA akuti ikuyembekezeka kutha mwezi wa NOVEMBER chaka chino.
Wofalitsa nkhani ku bungwe loona za sitima za pamtunda la Central East African Railways (CEAR) a Chisomo Mwamadi anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi.
Iwo ati ntchitoyi ikatha zithandiza kampaniyi kugwira bwino ntchito zake zotumikira a Malawi.
“Malo amenewa ndi amene akufuna kukhala malo athu ogwilira ntchito zosiyanasiyana. Atithandiza kuti sitima zizisempaha mosavuta chifukwa apapa ndi pakatikati penipeni pamene sitima zimasemphana kumapita ku nayuchi, ku kanengo, ku balaka komanso ku Blantyre. Zimenezi zitithandiza kuti tizitha kuchita transport katundu wochuluka,” anatero a Mwamadi.
Iwo ati padakali pano mu gawo lachiwirili, pamalopa pakumangidwa nyumba zokwana 32 za anthu omwe azigwira ntchito pa malopa.