Kudzipereka pa ntchito yakufalitsa uthenga wa Mulungu akuti ndi njira yokhayo imene imaonetsa chikhristu chenicheni.
Abusa Joseph Maganga a mpingo wa CCAP kuchokera ku Chiradzulu ndi omwe anena izi pofotokozera mtolankhani wathu. Iwo anati njira zofalitsira uthenga wa Mulungu ndi zambiri, ndipo ina mwa iyo ndi mawailesi a mipingo omwe tili nawo mdziko muno. Pamenepa m’busa Maganga wapempha akhristu kuti adzikonda kuthandiza Radio Maria yomwe nthawi zonse imakangalika kufalitsa uthenga wa Mulungu
Mwa zina m’busa Joseph Maganga pamodzi ndi akhristu ena kuchokera ku mpingo wa CCAP anayamikira maprogramu amene wailesiyi imaulutsa ponena kuti ndiwothandiza zedi.