Makolo a m’sungwana yemwe wakhala akuvutika ndi mthenda ya mtima ati ndiokondwa kaamba ka thandizo lamphamvu lomwe mwana wawo walandira mdziko la Italy.
Polankhula ndi Radio Maria Malawi Mai Catherine kajawo anathokoza bambo Josephy kimu omwe ndi a Director a Radio Maria Malawi pa thandizo lomwe anawachitira powapezera njira yabwino yokapezera thandizoli mdziko laItaly.
Mai Kajawo anati pa Iwo okha sangathe kuthokoza koma Mulungu yekha ndi yemwe angathe kubweza madalitsowo.
Ndipo pothokoza mulungu nsungwana yemwe wakhala akudwalayu Regina Kajawo anati pano ndiokondwa kaamba koti akutha kupanga chilichonse kusiyana ndi kale.