Mkulu owona zofalitsa nkhani , mauthega ndi kafuku-fuku ku bungwe la ma episikopi a mpingo wa katolika m’dziko muno laEpiscopal Conference Of Malawi (ECM) Ambuye George Desmond Tambalaapempha akhristu kuti agwirane manja potumikira mpingo wa katolika.
Ambuye Tambala anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi mu dayosizi ya Mangochipa mwambo wotsegulira maphunziro a masiku atatu a anthu omwe amagwira ntchito zofalitsa mauthenga, alembi a za uzimu ndi akulu-akulu a m’nyumba zosulira ansembe m‘ma dayosizi a mpingowu mdziko muno.
Iwo anatinso anthu akuyenera kuphunzitsidwa bwino pa kagwiritsidwe ntchito kabwino ka makina a Intaneti pofuna kupewa mavuto omwe amadza ngati anthu sakudziwa bwino kagwilitsidwe ka makina-wa.