Maanja pafupifupi khumi ndi asanu(15) akusowa pokhala nyumba zawo zitasasuka ndi mphepo yamphamvu mdera la Nswaswa kwa Mfumu yaikulu Mlumbe m’boma la Zomba.
Khansala wa delari a GANIZANI MALISHE watsimikizira Radio Maria Malawi za nkhaniyi ndipo wati mphepoyi yaononga denga la makalasi ndi tchalichi komanso nyumba za anthu.