Boma lapempha anamwino mdziko muno kuti azigwira ntchito yawo molimbika, mokhulupilika komanso modzipereka.
Nduna ya zaumoyo Dr. Peter Kumpalume apereka pempholi pa mwambo wopereka ma diploma ndi ma degree kwa ophunzira omwe atsiriza maphunziro awo ku sukulu ya ukachenjede ya unamwino ya Adventist m’boma la Ntcheu.
Iwo ati dziko lingapitite patsogolo ngati anthu ake ali ophunzira komanso ogwira ntchito molimbika ndi modzipereka.
Ndunayi yalangiza ophunzirawa kuti akagwire ntchito yawo mosakondera podzindikira kuti anthu odwala amafunika chisamaliro chokwanira ndipo awapempha kuti avomere kukagwira ntchito ngakhale madera akumidzi.
Dr. Kumpalume athokoza sukulu ya ukachenjede ya Adventist kaamba kogwirana manja ndi boma pa ntchito zokweza maphunziro mdziko muno.
M’mawu ake m’modzi mwa ophunzira omwe atsiriza maphunziro awo pa sukuluyi wati amadzindikira bwino kuti ntchito yachipatala ndi yothandiza anthu odwala choncho akayesetsa kugwira ntchito yake molimbika modzipereka komanso mosakondera.
Ophunzira omwe alandira ma diploma ndi madegree patsikuli ndi okwana mazana anayi 400 ndipo mutu wa mwambo watsikuli unali woti ‘Khalani Kuwala Kwa Dziko Lapansi’