Anthu makumi awiri (20) afa ndipo ena oposera zana limodzi (100) avulala modetsa nkhawa bomba litaphulika pa hotela ina mu m’dzinda wa las Vegas m’dziko la United States Of America.
Malipoti a BBCati bombali linaphulitsidwa kuchokera pamwamba pahotel-yo ndipo ena mwa anthu ena omwe anali kumaloko akuti anakwanitsa kuthawa ndipo apulumuka pa chiwembuchi.
Malingana ndi malipoti , munthu amene waphulitsa bombalo anamuzindikira ndipo waphedwa ndi apolisi pomuombera ndi mfuti.
Pakadali Pano apolisi akhadzikitsa ntchito yofufuza ena mwa anthu omwe akuwaganizira kuti akukhudzidwanso ndi chiwembuchi.