M’tsogoleri wa dziko lino Professor Arthur Peter Mutharika wafika m’dziko muno kuchokera mu m’dzinda wa New York , m’dziko la United States of America, komwe anachita nawo msonkhano wa ukulu wa bungwe la United Nations.
Mtsogoleri wa dziko linoyu President Mutharika wafika kuno ku mudzi pa 2 October 2017 kudzera pa bwalo la ndege la Kamuzu International mu m’dzinda wa Lilongwe.
Polankhula kwa atolankhani atangofika m‘dziko muno President Mutharika wati dziko la Malawi lipindula kwambiri ndi msonkhano-wu kamba koti wakwanitsa kukomana ndi magulu osiyanasiyana omwe alonjeza kuti afika ndi kudzathandiza pa ntchito zokweza dziko lino . Msonkhano-wu ndi wanambala 72 wa bungwe la United Nations unayamba pa 19 ndi kutha pa 25 September 2017.