M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse papa Francisco walimbikitsa akhristu a mpingo wakatolika pa dziko lonse kuti asafooke koma kudzipereka pochita mapemphero a Kolona tsiku ndi tsiku.
Papa Francisco walankhula izi mu uthenga wake wokhudza mwezi uno wa October, umene wati ndi ofunika kwambiri mumbiri ya mpingo-wu, kamba koti ndi mwezi wolimbikitsa mapemphero a kolona omwe ndi othandiza kwambiri pa moyo wa chikhristu pakati pa akhristu-wa.
Pamenepa iye wati mwezi wa October ukuyenelanso kukhala mwezi wopemphelera onse omwe akudzipereka pogwira ntchito zosiyanasiyana zothandiza pa chitukuko cha mpingowu ndi mayiko awo.