Apolisi ku Zalewa m’boma la Neno akusunga m’chitolokosi mai wina kaamba komuganizira kuti anapha mwana wake wongobadwa kumene.
Ofalitsa nkhani za apolisi m’bomali Sergeant Raphael Kaliati watsimikiza za nkhani-yi ndipo wati mayi-yu ndi Mary Lufaneti wadzaka 24 zakubadwa ndipo anachita izi pa 01 October 2017 pomwe anali oyembekezera ndipo itakwana nthawi yochira mayi-yu anapita pa thengo lina pomwe anakachilira ndipo mwanayo atabadwa anamumanga pa chitenje ndikumukwirira pomwepo.
Akuluakulu omwe amamuona mayi-yu ali woyembekedzera anali odabwa kumuona kuti analibe pathupi. ndipo atamufufuza iye anaulura kuti anamukwilira mwanayo pathengo.
Ndipo nkhaniyi itapita m’manja mwa apolisi iwo anamunjata mayi-yu ndipo pakadali pano ali m’manja mwa apolisi-wa kuyembekezeka kukayankha mulandu wakupha.
Mayi Mary Lufaneti amachokera m’mudzi mwa Kazunguza kwa mfumu yaikulu Mlauli m’boma la Neno.