Arch-Dayosizi ya mpingo wakatolika ya Blantyre yati ndiyokhudzidwa kwambiri ndi nkhanza zomwe zikupitilira kuchitika pakati pa amayi m’dziko muno.
Arch-Episikopi wa mpingowu mu Arch-Dayosizi-yi , Ambuye Thomas Luke Msusa , ndi amene wanena izi pa mwambo wa msembe ya ukaristia yokondwelera chaka cha umayi wa a mayi Maria, yomwe inakonzedwa ndi bungwe la amayi a chikatolika la Catholic Women Organisation mu Arch Dayosizi-yi.
Chaka cha umayi wa amayi maria cha mu arch dayosizi ya Blantyre chinachitikira kwa Mwanga Parish.