Akhristu a mpingo wakatolika mu dayosizi ya Mangochi awapempha kuti apitilize kudzipereka pothandiza mpingo-wu molowa manja .
Wachiwiri kwa m’tsogoleri wa dziko lino Dr Saulosi Chilima walankhula izi ngati mlendo wolemekezeka ku mwambo wa chaka chokondwelera nkhoswe ya dayosizi-yi.
Pamenepa Dr Chilima ati akhristu a mpingo wakatolika mu dayosiziyi akuyenera kuti avale zilimbe pothandiza mpingo-wu molowa manja ndi modzipereka kamba koti tsopano mpingo-wu uli m’manja mwawo chifukwa azungu omwe amathandiza mpingowu anabwelera kwawo.
Mwambo wa chaka cha nkhoswe ya dayosizi ya Mangochi chinayamba ndi mwambo wa msembe ya misa yomwe anatsogolera ndi a episikopi a mpingo-wu mu dayosizi-yi olemekezeka Ambuye Montfort Stima.
Mwazina akhristu-wa ku mwambo-wu athandizanso dayosizi yawo kudzera mu kugulitsa katundu wosiyanasiyana amene anabweletsa ndi cholinga chofuna kupeza ndalama zothandizira ntchito za dayosizi-yo.