Dziko la Mozambique lapulumutsa a Malawi 88 omwe likuwaganizira kuti anachita kuzembetsedwa ndi kuti azipita nawo m’dziko la South Africa.
Ofalitsa nkhani za department yoona za anthu olowa ndi otuluka ya immigration pa chipata cha Mwanza a Pasqually Zulu atsimikiza za nkhaniyi , ndipo wati anthuwo anawagwira ku Tete Province ali paulendo wopita m’dziko la South Africa , ndipo awatumiza m’dziko muno .
Iwo ati izi zachitika pa 5 mwezi uno. Anthu-wo akuti ndi a m’boma la Mangochi, Machinga ndi Balaka , ndipo mwa anthu-wo 8 ndi amayi , ndipo m’modzi ndi mwana.
anthu omwe anazembetsa anthuwo akuti ali m’chitokosi cha apolisi m’dziko la Mozambique , komwe ayimbidwe milandu yozembetsa , anthu Human Trafficking.