Mfumu yayikulu chikumbu ya m’boma la Mulanje yati sikugwilizana ndi m’chitidwe woti ana achitsikana azigwilitsidwa ntchito zovina pa miyambo ya zikwati kukhala ma (Dancing Queens).
Mfumuyi yalankhula izi pofotokozera mtolankhani wathu amene amafuna kumva zina mwa mapulani omwe mfumuyi ili nawo pa nkhani zotukula maphunziro a atsikana m’bomalo.
Mfumuyi yati itafufuza yapeza kuti m’chitidwe wolora atsikana kumavina mzikwati ngati ma Dancing Queens ndi umene ukukolezera zoti atsikana azikwati-wa msanga kamba koti zikumawapangitsa kuti azikhumbira zolowa mbanja adakali achichepere.