Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Apempha Boma kuti Lithandize ku Nkhanza zokhuzana ndi anthu a Khungu la Achialbino.

$
0
0

Bungwe la Association Of Person  With Albinism in Malawi lati likhala lokondwa likamva kuti anthu amene akukhudzidwa ndi milandu ya kupha ndi kuzunza anthu akhungu lachi alubino m’dziko muno awazenga milandu yawo.

President wa bungweli a Overstone Kondowe ndi omwe anena izi polankhula ndi mtolankhani wathu. Iwo ati ngakhale zikusonyeza kuti tsopano chitetedzo cha anthuwa chilibwino m’dziko muno, komabe bungwe lawo lizakhala lokondwa likamva kuti mabwalo a milandu ayamba kuzenga ndi kupeleka zilango zokhwima kwa anthu opezeka ndi milandu yakupha ndi kuzunza anthu a chi alubino-wa m’dziko muno.

A Kondowe anati ndizomvetsa chisoni pakadali pano kumaona anthu omwe analakwa pa milandu yokhudzana ndi kuzunza anthu a khungu lachi albino mdziko muno ndipo ati pakadali pano anthuwa anatulutsidwa mu ndende za dziko lino.

M’mawu awo iwo ati akhala okondwa atawona chilungamo chikuchitika pa milanduyi kaamba koti chilango chomwe amapatsidwa chimakhala chosagwira mtima chomwe amakhala atapha munthu koma akugamulidwa kuti akakhale kundende kwa zaka zisanu zomwe ndizosafana ndi moyo wa munthu.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>