Parish ya mpingo wakatolika ya Magomenero awayamikira kamba kodzipereka pa ntchito zotukula parishi-yo.
Bambo mfumu a parishi-yi , bambo Ignatius Bokosi , ndi omwe anena izi pomwe amafotokozera mtolankhani wathu zina mwa zitukuko zomwe akhristu-wo ayamba kulimbikitsa modzidalira.
Iwo ati akukhulupilira kuti zomwe akhristu-wa akuchita ndi zina mwa zimene akhala akuphunzira pa maulendo osianasiyana omwe akahala akuchita pokacheza ndi akhristu a mpingo-wu mma dayosizi ena.
Iwo ati mwa zina akhristuwo ayamba kumanga okha matchalitchi modzidalira komanso chaka chino apereka bwino masika zomwe zikusonyeza kuti akhristuwa ayambadi kudzipereka pa ntchito zotukula mpingo mu parishiyo.