Potsatira ngozi ya moto womwe wa sakaza katundu ndi nyumba yogona ophunzira pa Police Secondary School mu m’zinda wa Zomba, adindo okhudzidwa ndi nkhani-yi akhazikitsa komiti yofuna kupeza gwero la ngozi-yi.
Wofalitsa nkhani za apolisi m’chigawo chaku m’mawa kwa dziko lino Inspector Joseph Sauka wauza Radio Maria Malawi kuti mwa zina komiti-yi, yomwe yapangidwa ndi nthumwi zochokera pa sukuluyi, apolisi, a ESCOM, ndi a kuofesi yoona za ngozi zogwa mwadzidzi, ndinso a ku khonsolo ya mzindawu ithandizanso kupeza mulingo wa katundu amene wasakazika pa ngozi-yi. Ngozi ya kupsya kwa nyumba yogona ophunzira pa Police Boys Secondary School mu m’dzinda wa Zomba, yachitika dzana usiku ndipo yakhudza ophunzira 139 a pasukulu-yi.
Polankhula mkulu wa ku ofesi yozimitsa moto ya Fire Brigade mu khonsolo ya mzindawu a Leodins Sendaluzi wati anthu mukhonsoloyo akuyenera kumadziwitsa ofesi-yi mwansanga kudzera pa nambala ya 999 pogwilitsa ntchito nambala ya TNM kapena MTLkamba koti ndi yaulere.