Anthu atatu kuphatikizapo msungwana wa zaka khumi ndi zitatu amwalira atawombedwa ndi galimoto pa mtsinje wa Lunyangwa mumsewu wa Mzuzu-Karonga loweruka.
Malinga ndi mneneri wa apolisi mumzinda wa Mzuzu Sergeant Maurice Chapola pa nthawi ya ngoziyi dalaivala wa galimotolo lomwe nambala yake ndi CK 1960 Abraham Maseko wazaka 37 wa m’mudzi mwa Chinula, mfumu yayikulu Mtwalo mboma la Mzimba amachokera ku Mzuzu polowera ku Luwinga.
‘’Dalaivalayu atafika pa mtsinje wa Lunyangwa amafuna kupitirira galimoto lina lomwe linali kutsogolo koma ali mkati mochita izi anawona galimoto linanso kutsogolo kwake. Dalaivalayu anakhotetsera galimotolo kumbali kwa msewu komwe linawomba anthu anayi oyenda pansi kuphatikizaponso m’modzi wapa njinga yakapalasa ndipo galimotolo linatembenuzika ndikukagwera mumtsinje.’’ Atero a Chapola.
Malinga ndi a Chapola anthu atatu omwalirawo ndi Mary Phiri wazaka khumi ndi zitatu wa m’mudzi mwa Makhuwira mfumu yayikulu Mtwalo mboma la Mzimba, Queen Ndlove komanso bambo wina wa pa njinga yakapalasi yemwe sakudziwika dzina lake.
‘’Mwamuna wina m’modzi yemwe sakudziwika dzina lake wavulala kwambiri ndipo amugoneka pachipatala cha Mzuzu Central.’’ Atero a Chapola
Pakadali pano apolisi akufunafuna dalaivala wa galimotolo yemwe anathawa ngoziyo itachitika.