Akulu akulu omwe akuyendetsa zokonzekela za ulendo wa akhristu a ku Malawi opita kumalo oyera ku Rome mdziko la Italy pa 16 April chaka chino ati zokonzekera za ulendowo zili mkati ndipo zikuyenda bwino.
Polankhula lachinayi ku Maula Cathedral mu arch diocese ya Lilongwe pambuyo pokumana ndi akhristu omwe ali pa ulendowu Bambo Joseph Kimu omwe ndi mkulu wa mapulogalamu ku Radio Maria Malawi anati ulendowu ungakhale opambana ngati akhristuwa angazindikile koposa zaulendowu.
‘’Timasankhana maudindo ena ndi ena monga wapampando, mlembi, oyang’anira zakudya, azofalitsa nkhani, achipembezo, owona zachipatala ndi zina zotero. Ngakhale tilipo anthu 23 amene tikupita ku Rome tinaona kuti mchoyenera kuti gulu limeneli likhale ndithu lokonzekera bwino kuti aliyense azikachita zimene akuzidziwa.’’ Anatero Bambo Kimu.
Malinga ndi Bambo Kimu pa ulendowu akhristuwo akapemphera ku malo osiyanasiyana oyera.
‘’Ukoko kukakhala kuwona malo osiyanasiyana koma chachikulu chomwe titi tikakondwere kuchita ndi pa 27 April pamene Papa azalengeze kuti Papa Yohane 23 ndi woyera komanso Papa Yohane Paulo wachiri ndi oyera. Pa 28 April madzulo tizikanyamuka kubwerera kuno ku Malawi ndipo pa 29 ndi kumafika kunoko.’’ Anatero Bambo Kimu
Bambo Kimu anati ulendowu ndi wachinayi omwe akhristu akuno ku Malawi akhala akupita kunja ku malo osiyanasiyana oyera ndipo anati anthu ambiri omwe anapita mmaulendo amtunduwu akupereka umboni za madalitso ochuluka omwe akumalandira chifukwa cha maulendowa.
“Ulendo woyamba oyera ndinakonza mchaka cha 2000 pamene timakondwerera Jubilee ya zaka 2000 chibadwire Ambuye Yesu ndipo tinatenga anthu 62. Ulendo wachiwiri ndinakonza mchaka cha 2011, ndinatenga anthu 52 kupita ku Yerusalemu ndipo ulendo wachitatu mchaka cha 2012 ndinatenga anthu 47 kupita nawonso ku Yerusalemu. Tsopano uwu ndi ulendo wachinayi umene ndikuwatenganso anthu kupita ku Rome ndipo mwina chaka chamawa tizawatenganso anthu kupita ku Yerusalemu.” Anatsiriza motero Bambo Kimu.