M’tsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse papa Francisco wapempha akhristu kuti azikhala achikondi ndi olimba pa chikhulupiliro chawo.
Papa walankhula izi pomwe amathililapo ndemanga pa zakutchulidwa kwa akhristu 35 a mpingo-wu kuti ndi oyera.
akhristu-wa avomelezedwa pa 15 october ndi mpingo-wu kuti ndi oyera mu mpingo, pa mwambo waukulu , umene unachitikira pa bwalo La St Peters Square , ku likulu la mpingo-wu ku Vatican.
Oyera atsopano mu mpingowu , achokera m’mayiko a Brazil, Mexico, Spain ndinso Italy. mwa oyera atsopano-wa muli amsembe awiri.