Apolisi m’boma la Dowa amanga mzika za mdziko la Ethiopia khumi ndi m’modzi11 kaamba kolowa mdziko muno opanda chilolezo.
Wofalitsa nkhani za apolisi m’boma la Dowa, Sergeant Richard Kaponda wauza Radio Maria Malawi kuti apolisi agwira anthuwa ku malo osungirako anthu othawa kwawo a Dzaleka m’bomalo pamene anatsinidwa khutu ndi anthu ena kuti mzikazi zatsekeredwa mu nyumba ina ku malowa.
Apolisi atafika pa malopa ati anamanga anthuwa omwe anafotokoza kuti anatsekeredwa m’nyumbamo kuyambira pa 5 October chaka chino ndipo akhala akupatsidwa chakudya ndi mkulu wina yemwe sakudziwika.
Anthuwa omwe ndi a zaka zapakati pa 16 ndi 26ati amapita mdziko la South Africa kukasaka ntchito.
Padakali pano anthuwa akusungidwa ku ndende ya Maula podikira kuti apolisi afufuze bwino ndi kupeza munthu amene anawatsekera m’nyumbayo.