Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Chitukuko ndi cha Aliyense-Nankhumwa

$
0
0

Anthu m’dziko muno awapempha kuti achotse maganizo oti ntchito zachitukuko limayenera kugwira ndi boma.

 

Nduna ya za maboma ang’ono ndi chitukuko cha kumidzi olemekezeka a Kondwani Nankhumwa ndi omwe anena izi atangomaliza kuyendera ntchito ndi zitukuko zomwe bungwe la Icelandic Development Agency (ICEDA) likulimbikitsa m’boma la Mangochi .

Iwo ati kutenga gawo pa ntchito za chitukuko ndi njira yokhayo yomwe ingathandize pa chitukuko cha dziko lino.

“Pali ntchito zambiri zoti tigwire ndiye boma silingakwanitse zonse palokha timafuna anthu enanso komanso mabungwe kuti atithandize pogwira ntchito ngati zimenezi,”anatero a Nankhumwa.

Pamenepa ndunayi inayamikira  ntchito zapamwamba zomwe bungwe la ICEDA lakhala likulimbikitsa maka kumbari ya zomangamanga ndi zina zambiri  m’bomalo.

A Nankhumwa anati boma lili ndi chidwi chochita zitukuko zambiri mmadera akumidzi kamba koti anthu ambiri omwe ndi pafupifupi 90 percent amakhala madera akumudzi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>