Bungwe lomenyera ufulu wa atolankhani m’dziko muno la Media Institute Of Southern Africa (Misa-Malawi) layamikira atolankhani momwe akugwilira ntchito zawo pofalitsa mauthenga okhudza mpheketsera yokhudzana ndi nkhani zopopa magazi zomwe zakhala zikumveka m’mamboma ena m’dziko muno.
Wapampando wa bungwe-li a Tereza Ndanga , ndi amene wanena izi polankhula ndi mtolankhani wathu amene amafuna kumva ndemanga za bungweli , pa za momwe atolankhani agwilira ntchito zawo pofalitsa nkhani zokhudza mpheketsela ya zopopa magazi-yi m’dziko muno. Ndanga wati bungwe la Misa kuno ku Malawi liyesetsa kupeleka ukadaulo woyenera wofalitsira nkhanizi kwa atolankhani m’dziko muno.