Vuto la kusowa kwa magetsi m’sukulu za ku midzi akuti ndi limene likukoledzera mavuto a kusachita bwino pakati pa ophunzira m’sukuluzi pa maphunziro awo.
Wachiwiri kwa m’phunzitsi wa mkulu pa sukulu ya sekondale yoyendera ya Bvumbwe , m’boma la Thyolo , a Damiano Kondowe , ndi omwe anena izi polankhula ndi mtolankhani wathu. Iwo ati ana ambiri a msukuluzi amakhala ndi mzeru zokwanira , koma kuti amalephera kukonzekera bwino mayeso awo , kamba ka vuto la magetsi , panthawi yomwe afuna kuti awerenge nthawi ya usiku. Iwo apempha boma kuti pomwe likulimbikitsa zitukuko zosiyanasiyana m’dziko muno lilimbikitsenso ntchito yopatutsa nthambo za magetsi kuti zifike msukuluzi , kuphatikizaponso ya Bvumbwe CDSS , yomwe ndi imodzi mwa sukulu zakale , koma kufikira pano ilibe magetsi. Iwo ati ngati boma lingachite izi ndiye kuti ana ambiri a msukuluzi azichita bwino pa maphunziro awo.