Apolisi mchigawo cha kummawa kwa dziko lino ati akuchita chotheka kuwonetsetsa kuti anthu mchigawochi akulandira chitetezo chokwanira.
Wofalitsa nkhani za apolisi mchigawochi Inspector Joseph Saukawauza Radio Maria Malawi kuti potsatira mphekesera yakuti anthu ena akumalemba nyumba za anthu ndi zinthu za mtundu wofiyira ngati magazi.
Iwo ati apolisi atachita kafukufuku ngakhalenso achipatala apeza kuti zinthuzo si magazi, komabe apolisiwa akhazikitsa kafukufuku wofuna kudziwa anthu omwe akuchita mchitidwewu komanso zolinga zawo ndipo kuti akagwidwa lamulo ligwira ntchito pa iwo.
Inspector Sauka amemeza anthu mchigawochi kuti asiye kukhala mwa mantha kaamba koti apolisi akugwira ntchito yawo. Apolisi apempha anthu mchigawochi kuti akanene ku polisi ngati atakhala ndi uthenga okhudza anthu omwe akuchita mchidwewu.