Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Apolisi Akusaka Dalaivala Yemwe Wapha Munthu ndi Kuthawa

$
0
0

Apolisi m’boma la Ntchisi akufunafuna oyendetsa galimoto wina yemwe wapha munthu atamuwomba ndi galimoto ndikuthawa.      

Malinga ndi ofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Sergeant Gladson M’bumpha, ngoziyo, yachitika lachitatu pa 15 November, pomwe galimotolo, lomwe pano silidadziwike limachokera mbali ya Nkhotakota kupita ku Kasungu komwe omwalirayo a Chrispine Kafere a zaka 25 zakubadwa amachokera ali pa njinga yakapalasa.

Sergeant M’bumpha wati ngoziyo itachitika zikuonetsa kuti dalaivala wa galimotolo sadaime atavulaza kwambiri mkuluyo m’mutu.

Pakadali pano kafukufuku wa apolisi akupitilira kuti agwire oyendetsa galimotolo.

Malemu Kafere, anali wa m’mudzi mwa Chipwaila, mdera la mfumu yaukulu Chilooko m’boma lomwelo la Ntchisi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>