Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

PULEZIDENTI BANDA WATI A MUTHARIKA ANAYAMBITSA ZIWAWA KU THYOLO

$
0
0

Pulezidenti Dr Joyce Banda wati ziwawa zomwe zinachitika kwa Goliati mboma la Thyolo sabata yatha zomwe zinazetsa imfa ya wapolisi ndi munthu wamba m’modzi zinakonzedwa ndi pulezidenti wachipani cha Democratic Progressive [DPP] Proffessor Peter Mutharika.

Poyankhula mboma la Zomba pamsonkhano wachipani chawo cha Peoples Pulezidenti Banda anati ali ndi umboni wokwanira kuti a Mutharika ndi omwe anamemeza anthu otsatira chipani chawo kuti achite ziwawazo.

Malinga ndi Pulezidenti Banda a Mutharika anakachititsa msonkhano wawo lachisanu pa malo omwe iwo anakachititsapo msonkhano wawo la Mulungu lotsatira.

‘’Zinthu zoyipazi anachita ndi a DPP motsogoleredwa ndi a Mutharika. Anthu onse omwe anachita zimenezi ayenera kulandira chilango,’’ anatero Dr Banda.

Poyankhula pa msonkhano wa atolankhani omwe anachititsa mumzinda wa Blantyre Pulezidenti wachipani cha DPP Proffessor Mutharika wati chipani chake sichikukhuzidwa ndi zipolowezi.

Mutharika wati akukhulupirira kuti mchitidwe wa zipolowe ungathe ngati mabungwe a Public Affairs Committee [PAC] komanso Malawi Electoral Commisssion [MEC] atatenga gawo lalikulu poyitanitsa zipani ndi kukambirana.

“Ndikupempha atsogoleri andale tisamayankhule zinthu zomwe zimapangitsa anthu kupsa mtima, tatsala ndi masiku 60 kuti tichite zisankho,zisankho zitha ndipo ife tipitilira kukhala ndiye tigwirizane.Bungwe la PAC linathandiza mchaka cha 1993 kuti mdziko muno mukhale zisankho zabwino ndiye mutafunsa iwowa athandize”,atero a Mutharika.

A Mutharika ati akufuna kuchita kampeni ya bata ndi yosanyozana kamba koti ali ndi chikhulupiriro kuti a Malawi adzasankha okha boma lomwe akufuna ndipo wati  ndi okonzeka kuzavomereza zosatira za chisankhocho.

Komabe a Mutharika adzudzula chiwembu chomwe anthu ena anachitira m’modzi mwa mamembala achipani cha DPP yemwenso ndi wothandizira ofesi yawo a BEN PHIRI ku nyumba yogona alendo ya Mount Soche mumzinda wa Blantyre lolemba sabata yatha. A Mutharika ati akuganiza kuti anachita zamtopolazi ndi anyamata a chipani cholamula cha PEOPLES.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>