Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Mnangagwa Akuyembekezeka Kukhala Mtsogoleri wa Zimbabwe

$
0
0

Yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wadziko la Zimbabwe a Emmerson Mnangagwa akuyembekezeka kulumbilitsidwa kukhala mtsogoleri wa dzikolo posachedwapa kutsatira kutula pansi udindo kwa yemwe anali mtsogoleri wa dzikolo a Robert Mugabe.

Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, Mnangagwa yemwe masabata awiri apitawa anathawira mdziko la South Africa powopa kuchitidwa chipongwe ndi otsatira a Mugabe, akuyembekezeka kufika mdzikomo lero.

Kuchotsedwa pa mpando kwa a Mnangagwa kunadzetsa mpungwepungwe mdzikomo zomwe zinachititsa kuti asilikali a dzikolo alowelerepo kufikira pamene a Mugabe atula pansi udindo wawo.

A Mugabe alengeza za kutula pansi udindo kwawo kudzera mu kalata yomwe inawerengedwa mu nyumba ya malamulo ya dzikolo pamene aphungu analinso mkati mochita ndondomeko zochotsera a Mugabe pampando mokakamiza.

Malipoti ati anthu onse mdzikolo anachita chikondwelero usiku onse wa lachiwiri atamva za kutula pansi udindo kwa a Mugabe.

Koma mu kalatayo, a Mugabe ati atula pansi udindowo mwa kufuna kwawo pofuna kupereka mpata kuti pakhale kusinthana mphamvu zolamulira dzikolo mwa bata ndi mtendere.

Malipoti ati mnangagwa yemwe ali ndi zaka 71, yemwe akuyembekezeka kulumbilitsidwa lero lachitatu kapena mawa lachinayi alamulira zaka zotsala za a Mugabe kufikira nthawi ya zisankho zomwe zichitike mwezi wa September chaka cha mawa.

Koma malinga ndi malamulo oyendetsera dzikolo, yemwe akuyenera kulamulira dzikolo padakali pano ndi a Phelekezera Mphoko yemwe anali wachiwiri kwa mtsogoleri wa dzikolo atachotsedwa a Mnangagwa koma zikukayikitsa ngati ali mdzikomo pamene pakumveka mphekesera kuti akuluakulu a chipani cha ZANU-PF achotsa mkuluyu pa mpandowu.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875


<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>