Bwalo loyamba la milandu m’boma la Ntchisi lalamula bambo wina wa zaka 46 zakubadwa kuti akakhale ku ndende ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga kwa zaka zisanu ndi zitatu (8) litamupeza olakwa pa mlandu ogwililira ndi kupereka pathupi kwa msungwana wina ozelezeka wa zaka 20 zakubadwa.
Wofalitsa nkhani za apolisi m’bomalo Sergeant Gladson Mbumpha wati zinazindikirika kuti msungwanayu Salome Chiwanda ali ndi pathupi mwezi wa October chaka chino ndipo atamufunsa ndi pomwe anatchula mkuluyu Laudan Jamu kuti ndiyemwe wamupatsa pathupipo.
Akuluakulu a m’mudzimu anakanena za nkhaniyi ku polisi zomwe zinachititsa kuti mkuluyu amangidwe ndipo atafunsidwa ku bwalo la milandu, mkuluyu anauvomera mlanduwu.
Popereka chigamulo chake First Grade Magistrate Dorothy Kalua anati mlanduwu ndi waukulu kwambiri kaamba koti anagona ndi msungwana yemwe ndi wozelezeka choncho akuyenera kulandira chilango chokhwima ndipo anamulamula kuti akakhale ku ndende ndi kukagwira ntchito ya kalavulagaga kwa zaka zisanu ndi zitatu (8) kuti enanso omwe ali ndi khalidwe loyipali atengerepo phunziro.
Laudani Jamu amachokera m’mudzi mwa Azolo mfumu yaikulu Chilooko m’boma lomwelo la Ntchisi.