Yemwe akuyembekezeka kukhala mtsogoleri wa dziko la Zimbabwe a Emmerson Mnangagwa wati akufuna kuti dzikolo likhale latsopano lomwe anthu ake akhale ndi ufulu wawo wachibadwidwe.
Malinga ndi malipoti a wailesi ya BBC, Mnangagwa amalankhula izi ku likulu la dzikolo ku Harare atangofika kumene kuchoka mdziko la South Africa kutsatira kutula pansi udindo kwa a Mugabe omwe anali mtsogoleri wa dzikolo kwa zaka 37.
Mnangagwa walonjeza kukweza chuma cha dzikolo, kudzetsa mtendere mdzikomo komanso kupereka mwayi wa ntchito kwa anthu a mdzikolo pamene malipoti akusonyeza kuti anthu 90mwa 100 aliwonse sali pa ntchito mdzikolo.
Mkuluyu yemwe akuyembekezeka kulumbilitsidwa kukhala mtsogoleri wa dzikolo mawa lachisanu, wayamikira asilikali a dzikolo pothandizira kuchotsa a Mugabe pampando mwamtendere.
A Mugabe omwe padakali pano ali ndi zaka 93 ati atula pansi udindowo mwa kufuna kwawo pofuna kupereka mpata wosinthana ulamuliro wa dzikolo mwa bata ndi mtendere.