Mchitidwe wosalana kaamba ka kusiyana pa zipembedzo ati ungathe mdziko muno ngati akhristu komanso asilamu akhala omvetsetsana mu zochita zawo.
Mphunzitsi wa phunziro la chisilamu pa sukulu yosulira ansembe ya Inter-Congregation Institute (ICI) m’boma la Balaka, bambo Voni Boxel anena izi pambuyo pa ulendo omwe asemino a pa sukuluyi anali nawo womwe anayendera ndi kukaphunzira zina zokhudza chipembedzo cha chisilamu pa mzikiti waukulu m’boma la Balaka.
Iwo ati kusiyana pa zipembezo si chifukwa choti ena azikhala mwa mantha ndipo apempha anthu mdziko muno kuti akhale zida zodzetsa umodzi komanso mtendere posatengera chipembedzo kapena zikhulupiliro zawo.