Banki yaikulu m’dziko muno ya Reserve yayamikira banki yaikulu padziko lonse ya World Bank kaamba ka thandizo lachuma lomwe limapereka pa chitukuko cha dziko muno.
Mkulu wa banki-yi m’dziko muno a Dalitso Kabambe anena izi lachinai mu mzinda wa Lilongwe, pamene a banki yaikulu padziko lonse amakhazikitsa malipoti atatu akuluakulu okhudza kayendedwe ka chuma cha dziko lino.
Iwo ati malipotiwa abwera pa nthawi yake pamene dziko lino likulimbana ndi nkhani zakubedwa kwa ndalama za boma, kutsika mphamvu kwa ndalama komanso kusinthasintha kwa nyengo mwazina zomwe zokhudza kwambiri dziko lino zaka zapitazi.
A Kabambe ati ndalama ya kwacha yakhazikika pakati pa miyezi 12 ndi 15 yapitayi zomwe zikupereka chilimbikitso pazatsogolo la chuma cha dziko lino.
M’mawu ake oyimilira banki yaikulu padziko lonse mdziko muno a Greg Toulmin wati chuma cha dziko lino changathe kupita patsogolo boma litachilimika potsogolera ntchito za alimi ang’onoang’ono ndi aakulu omwe.
Ina mwa malipotiwa akuwunika momwe vuto la kusintha kwa nyengo kwakhudzila chuma cha dziko lino.