Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Anthu Aleke Kuchitirana Nkhanza

$
0
0

Anthu mdziko muno awapempha kuti aleke kuchitirana nkhanza wina ndi mzake komanso makamaka m’mabanja.

Mkulu wa apolisi mchigawo cha kum’mawa kwa dziko lino, Commissioner Martha Suwedi ndi yemwe wanena izi ku Chinamwali m’boma la Zomba pa ulendo wa ndawala womwe apolisi achizimayi anayenda pakuyamba kwa masiku 16 othetsa nkhanza za m’banja.

Iye wachenjeza onse ochitira nkhanza amayi pa kuwagwililira komanso kuwamenya kuti alekeretu kaamba koti  apolisi sadzalekelera mchitidwewu koma kumanga aliyense opezeka akuchitira amayi nkhanza.

Polankhulapo, wapampando wa bungwe la apolisi a chizimayi la Police Women Network mchigawo cha kum’mawa Assistant Supretendent Josophine Chigawa wati cholinga chawo ndi chofuna kuwonetsetsa kuti nkhanza za m’banja zatheratu mchigawochi.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>