A Malawi akhala ndi mwayi olemba nawo Baibulo la Chichewa pa manja lomwe likasiyidwe ku malo omwe amasungirako ma Baibulo mdziko la Israel.
Malinga ndi mkulu yemwe akuyendetsa ntchitoyi mdziko muno yomwe ikutchedwa kuti Bible Valley a Clapperton Mayuni, ati dziko lino likhala limodzi mwa mayiko 1 hundred omwe mzika zake zilembe nawo ndime zosiyanasiyana zopezeka mu Baibulo ndikukonza Baibulo lolembedwa pa manja mu zilankhulo zawo.
Poyankhula pa msonkhano wa atolankhani mumzinda wa Blantyre a Mayuni ati ntchitoyi igwirika mzigawo zonse za dziko lino ndicholinga choti a Malawi ambiri adzakhale ndi mwayi olemba nawo mu Baibulolo.