Quantcast
Channel: Radio Maria Malawi
Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

PULEZIDENTI BANDA WAKHUTIRA NDI MMENE MALONDA A FODYA AYAMBIRA

$
0
0

Pulezidenti Dr Joyce Banda wati ndi okondwa ndi mitengo yomwe alimi anagulitsira fodya wawo lolemba pamene amatsekulira msika wambewuyi chaka chino ponena kuti akukhulupirira kuti chaka cha 2014 chikhala cha mayankho kwa alimi afodya mdziko muno.

Polankhula ku Kanengo mumzinda wa Lilongwe potsekulira msika wa fodya wa mchaka cha 2014 Pulezidenti Banda wayamikiranso alimi chifukwa cholima fodya wapamwamba zomwe wati zithandiza kuti alimi asakumane ndi mavuto obwezedwa ku msika kuti akasankhenso fodya wawo moyenera.

“Ndayendera msika wa fodya ndi magulu anayi afodya kuphatikizapo fodya yemwe amalimidwa kudzera ku ndondomeko ya boma komanso wa alimi wamba. Ndakhutira powona kuti fodya wa ndondomeko ya boma alimi agulitsa kufika pa 2 dollars 90 cents ndipo ndawonanso kuti fodya winayu alimi agulitsa pa 2 dollars 5 cents[K833],’’ anatero Pulezidenti Banda.

Komabe pulezidenti Banda wapempha makampani ogula fodya kuti awonesetse kuti akugula fodya pa mitengo yokwera pofuna kuti alimi omwe achita khama polima mbewu yapamwamba ya fodya apeze cholowa.

M’mawu ake mkulu wa bungwe la Tobacco Control Commission [TCC] a Bruce Munthali anati bungweli lili ndi chiyembekezo choti dziko lino likhala ndi fodya wochuluka pafupifupi makilogalamu 193 miliyoni.   

Dziko la Malawi limadalira kwambiri fodya pa chuma chake. Mchaka cha 2013 kampani ya Auction Holdings Limited inagulitsa fodya wa mitundu yosiyanasiyana wolemera makilogalamu 169 miliyoni ndipo ndalama pafupifupi 362 miliyoni Dollars ndi zomwe zinapezeka kuchokera ku malonda a fodya.


Viewing all articles
Browse latest Browse all 1875

Trending Articles


Mdima unadetsa dziko



<script src="https://jsc.adskeeper.com/r/s/rssing.com.1596347.js" async> </script>