Pamene dziko la South Africa likuyembekezeka kusankha mtsogoleri watsopano wa dzikolo mchaka cha 2019, malipoti akusonyeza kuti wachiwiri kwa pulezidenti mdzikolo Cyril Ramaphosa,ndi yemwe ali ndi mpata waukulu odzatenga udindowu.
Pakadali pano Ramaphosa ndi yemwe akutsogola pazisankho za mzigawo zomwe chipani cholamula cha African National Congress ANC, chikuchititsa pofuna kupeza atsogoleri ake atsopano pokonzekera chisankho cha mtsogoleri wa dziko.
Pa udindo wa pulezidenti wachipani, a Ramaphosa akupikisana ndi mai Nkosazana Dlamini Zuma omwenso anali mkazi wa pulezidenti Zuma,ndipo opambana ndi yemwe adzaimilire chipanichi pa chisankho cha mu 2019.
Izi zikuchitika pamene mtsogoleri wa dzikolo Jacob Zuma akudzapuma paudindo wake mchaka cha 2019.