Ntchito za maphunziro ati sizikuyenda bwino pa sukulu ya sekondale yoyendera ya Mbombwe m’boma la Mangochi potsatira kuchepa kwa aphunzitsi pa sukuluyo.
Mphunzitsi wamkulu pa sukuluyi a Rodgers Tiwonge Mpinganjira, ndi omwe anena izi polankhula ndi Radio Maria Malawi.
Iwo ati sukuluyi ikugwira ntchito ndi mphunzitsi m’modzi yekha yemwe ndi mphunzitsi wamkuluyu, kaamba koti aphunzitsi ena anali a ku pulaimale ndipo anapita ku sukulu za ukachenjede kokawonjezera maphunziro awo.
Ndipo polankhulapo, mkulu wa ku ofesi yoona za maphunziro m’bomalo aJoe Magomboati ofesi yawo, ikudziwa za vutoli ndipo iwonetsetsa kuti sukuluyi ithandizidwe posachedwapa.