Mtsogoleri wa mpingo wakatolika pa dziko lonse Papa Francisco wapempha anthu kuti alemekeze ganizo la bungwe lowona za mgwirizano wa maiko a pa dziko lonse la United Nations lokhazikitsa mzinda wa Yerusalemukukhala likulu la dziko la Israel.
Polankhula lero pa mkumano omwe amalankhala nawo lachitatu lililonse ndi anthu osiyanasiyana omwe amakayendera likulu la mpingo wakatolikali, Papa wati kukhazikitsidwa kwa mzindawu kukhala likulu la dziko la Israel, ndi njira imodzi yobweretsa mtendere kamba koti mu mzindawu muli malo oyera a anthu a chipemmbedzo cha chisilamu, ayuda ngakhalenso akhristu.
Malipoti a wailesi ya Vatican ati atsogoleri a mmaiko a mchigawo chapakati cha kuvuma achenjeza kuti izi zichititsa kuti pakhale chisokonezo komanso zamtopola.