Anthu atatu afa ndipo ena khumi ndi m’modzi (11) avulala pa ngozi ya pa nsewu yomwe yachitika pa Mtengowanthenga m’boma la Dowa.
Wofalitsa nkhani za apolisi pa polisi ya Mponela m’bomalo, Sub Inspector Kondwani Kandiado watsimikiza za ngoziyi ndipo wati tayala la galimotoli linachoka m’malo mwake ndipo chifukwa choti galimotolo linali pa liwiro lamphamvu linakanika kuyima ndipo linagudubuzika katatu.
Iye wati anthu asanu omwe avulala kwambiri pa ngoziyi awatengera ku chipatala cha Kamuzu Central mu mzinda wa Lilongwe ndipo mwa atatu omwalirawa ndi msilikali wa ku Kamuzu Barracks komanso mwana wachichepere.