Bwalo loyamba la milandu mboma la zomba lalamula bambo wina wa zaka 35 zakubadwa kuti akakhale ku ndende ndi kukagwira ntchito ya kalavula gaga kwa zaka zisanu ndi zitatu (8) atamupeza olakwa pa mlandu wogwililira mwana wake womupeza wa zaka khumi ndi zitatu (13).
Bwaloli linamva kuti mkuluyu, John Master masana wa pa 18 November chaka chino anamuitanira mwanayo mnyumba ndi kumuvula ndi kuyamba kuchita naye za dama. Mwanayu anakuwa ndipo anthu anakhamukira mnyumbayi ndi kugwira mkuluyu kupita naye ku polisi ya Jali m’bomalo ndipo mwanayu atamutengera kuchipatala zinakatsimikizika kuti wagwiliridwa.
Mkulu woyimira boma pa mlandu Sub Inspector Gerald Chinoko anapempha bwaloli kuti limpatse mkuluyu chilango chokhwima kaamba koti ngati bambo, ndi udindo wake woteteza mwana wa mkazi komanso pakadali pano mwanayo ubongo wake wasokonekera.
Ndipo podandaula mkuluyu anapempha bwaloli kuti limupatse chilango chofewerako kaamba koti ndi koyamba kupalamula komanso ndi yemwe amasamalira banja lake.
Koma popereka chigamulo chake First Grade Magistrate Asunta Muwalo, anagwirizana ndi mkulu woyimira boma pa mlanduyu powonjezera kuti zomwe anachita mkuluyu ndi zosemphana ndi gawo 138 la buku la malamulo a dziko lino ndipo analamula mkuluyu kukakhala ku ndende kwa zaka zisanu ndi zitatu (8) kuti ena atengerepo phunziro.
A John Master amachokera m’mudzi mwa Jeremani mfumu yaikulu Chikowi m’boma lomwelo la Zomba.