Anthu oposa 170 afa ndipo ena ambiri avulala pakumenyana kwa pakati pa mitundu iwiri ya anthu mdziko la South Sudan.
Malipoti a wailesi ya BBC ati anthu oposa 200ndi omwe avulala pa kumenyanaku komwe kukuchitika mdera la kuzambwe kwa nyanja ya dzikolo.
Ngakhale nkhondo zapachiweniweni zili zochulukira mdzikolo, nkhondoyi ati ndi imene yaphetsa anthu ambiri zomwe zachititsa mtsogoleri wa dzikolo Salva Kiir kulengeza kuti dziko la South Sudan ndi dziko la ngozi. A Kiir alamulanso asilikali a dzikolo kuti agwiritse ntchito mphamvu pothetsa kumenyanako ngati anthuwa satula pansi zida zawo mwamtendere. Malipoti ati nyumba zokwana 342 zawotchedwa ndipo anthu pafupifupi 1800 ndi momwe akusowa pokhala kaamba ka nkhondoyi.