Bungwe lomenyera maufulu a wanthu pa dziko lonse la Amnesty Internationalladzudzula maiko a ku ulaya kaamba kozunza komanso kuchitira nkhanza anthu othawa kwawo a mdziko la Libya.
Malinga ndi malipoti a waliesi ya BBC, bungwe la Amnesty Internationallapeza kuti ngati njira imodzi yothana ndi vuto la anthu othawa kwawo, maikowa akumazunza anthu othawa kwawo popereka ndalama kwa asilikali komanso anthu ozembetsa anzawo kuti agwire ntchitoyo.
Dziko la Libya ndi limodzi mwa maiko omwe anthu ambiri amadzera akafuna kupita m’maiko a ku uluya pogwiritsa ntchito njira ya pamadzi kukafika m’maikowa.
Bungweli lati alonda omwe anaikidwa m’mbali mwa nyanjayi ayamba kugwira ntchito ndi zigawenga komanso anthu ozembetsa anzawo omwe akumazunza kwambiri anthuwa.